Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la MEC Lichititsa Chisankho Chapadera

$
0
0

Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lachiwiri lichititsa chisankho chapadera cha makhansala mmadera asanu  momwe mulibe makhansala pazifukwa zosiyanasiyana mdziko muno.

 

Muuthenga omwe bungweli latulutsa, wapampando wabungweli  Justice Maxon Mbendera SC, wati anthu okhawo omwe analembetsa mu kaundula wa voti m’madera omwe kuli chisankho ndi omwe akuyenela kukaponya voti.

 

Justice Mbendera wati pachisankhochi bungwe la MEC layikanso ndondomeko zomwe zithandize anthu olumala, amayi oyembekezela, okalamba ndi odwala kuti akavote mosavutikira.

 

Mundondomekoyi,bungweli lapempha anthu ogwira ntchito mmalo oponyera voti kuti athandize anthuwa powapatsa mwayi osayima panzere ndi cholinga choti aponye voti yawo mwachangu.

 

Bungweli lati anthu omwe ali ndi vuto losawona alinso ndi mwayi operekezedwa ndi munthu yemwe adalembetsa mu kaundula wa voti pachisankhochi kuti akawathandizire posankha munthu yemwe akumufuna pogwiritsa ntchito chikombole cha mabowo anayi chothandizira anthuwa povota.

 

Anthu omwe akuyembekezeka kuvota pachisankhochi mmadera onse asanu ndi 27,272. Malinga ndi Justice Mbendera zotsatira zachisankhochi zikuyembekezeka kudzalengezedwa lachitatu pa 26 sabata ino.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>