Kusadziwa komanso ulesi opita kuchipatala kukayezetsa nthenda ya Cancer ndi zina mwanjira zomwe zikupititsa patsogolo chiwerengero cha anthu odwala matendawa m'dziko muno.
M'modzi mwa madotolo akuluakulu a zachipatala Dr Getrude Sambakunsi ndi omwe anena izi mu mzinda wa Blantyre pofotokozera mtolankhani wathu yemwe amafuna kudziwa zina mwa njira zomwe zikuchititsa kuti nthenda ya Cancer izitenga miyoyo ya anthu yochuluka masiku ano.
Dr Sambakunsi ati ndi zomvetsa chisoni kuti kufikira pano anthu ochuluka sadziwa zambiri zokhudza matendawa komanso alibe chidwi chofuna kudziwa momwe thupi lawo likugwilira ntchito.
Pamenepa Dr Samvakunsi ati nthendayi imavuta kwambiri ikazindikiridwa mochedwa.
Iwo apempha a Malawi kuti ngati njira imodzi yothanira ndi nthendayi, anthu akuyenera kumaonana ndi madotolo pafupipafupi makamaka ngati awona zizindikiro zina zodabwitsa pathupi lawo.