Mtsogoleri wa Mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapepesa Pulezident wa dziko la Romania potsatira ngozi ya moto yomwe yapha anthu makumi atatu ndi awiri, ndikuvulaza ena 130 mu m’dzinda wa Bucharest m’dzikolo.
Papa wati ndi wokhuzidwa chifukwa mwa anthu omwe amwalira komanso kuvulala ndi anyamata ndipo wati alimbikitsa mapemphero ku m’maanja omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati motowo unayamba kamba ka mphamvu ya magetsi yomwe bandi yomwe imasangalatsa anthu patsikulo imagwiritsa ntchito.