↧
Anthu khumi ndi m’modzi avulala pa ngozi ya galimoto m’boma la Ntchisi.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergent Gladson Mb’umpha wati pa anthu omwe avulalawo, anayi avulala kodetsa nkhawa ndipo akulandira thandizo pa chipatala chachikulu cha m’bomalo, pomwe mayi m’modzi amutumiza ku chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe.
Galimotolo ati lachita ngoziyi kamba koti dalaivala yemwe amayendetsa galimotolo analephera kuwongolera kamba ka vuto la ma buleki.
Dalaivalayo ndi Benson Ching’ombe, pomwe galimoto lomwe amayenetsalo ndi la mtundu wa Toyota Hilux , nambala yake ndi NS 479 ndipo linanyamula anthu khumi ndi asanu omwe amapita ku maliro .