Kampani yogulitsa mbeu mdziko muno ya Mosanto Malawi yachenjeza alimi kuti apewe kugula mbeu kwa mavendor.
Mkulu wa zamalonda ku kampaniyi a Denis Kachikho ndi omwe anena izi potsatira kumangidwa kwa a Mavuto Chilipa omwe apolisi anawapeza akugulitsa mbeu yowonongeka ya chimanga pa nsika wa Bvumbwe m’boma la Thyolo.
A Kachikho ati ma venda nthawi zina amapezeka ndi katundu wosayenera choncho ndi kofunika kuti alimi asamagule mbeu zawo.
Iwo apemphanso boma kuti liwunikenso malamulo ogulitsira mbeu ndi cholinga choti aliyense wopezeka akugulitsa mbeu yowonongeka azipatsidwa chilango chokhwima.
Pamenepa Iwo ati mchitidwe wotere umabwezera m’mbuyo chitukuko ndinso njala m’dziko muno.