Nsika wa Kasungu omwe unapsa mwezi wa October ati ukufunika ndalama zoposa 10 Million Kwacha kuti ukozedwenso.
Wachiwiri kwa Meya wa Manicipality ya Kasungu a Ephate Joshua ndi yemwe wanena izi pomwe kampani yopanga cement ya Shayona imapereka matumba a cement okwana 1 hundred 20 ku khonsoloyi ndi cholinga chothandizira ntchito yokonzanso msikawu.
A Joshua ati motoyu unaononga zinthu zambiri kuphatikizapo maofesi ena a khonsoloyi ndipo pafunika ndalama zokwana 10 million kwacha kuti zinthu zibwerelenso m`chimake.
Iwo ati padakali pano khonsoloyi ikulephera kutolera misokho mumsikawu zomwenso zikubwenzeretsa ntchito zake m`mbuyo.
M`mawu ake m`modzi mwa akuluakulu a kampani ya Shayona a Austin Mvula anati apereka thandizoli kamba koti anamva za ngoziyi.