Mtsogoleri wa dziko la Rwanda Paul Kagame wadzudzula ziwawa zomwe zikuchitika m`dziko la Burundi zomwe zikuphetsa anthu ankhanikhani.
Pulezidenti Kagame wati anthu m`dzikolo akungophedwa mwachisawawa tsiku lililonse komanso matupi a anthu akufa akungopezeka mmisewu ya mdzikolo.
Izi zadza potsatira chenjezo la pulezidenti wa dziko la Burundi a Pierre Nkurunziza omwe anati athana ndi wina aliyense yemwe amatsutsa mfundo zoyendetsera dzikolo.
Zipolowe m`dziko la Burundi zinayamba m`mwezi wa April chaka chino pomwe Pulezidenti wa dzikolo analengeza kuti ayimanso kachitatu pa mpandowu zomwe ndi zosemphana ndi malamulo oyendetsera dzikolo.