Atolankhani mdziko muno awapempha kuti azilemba nkhani zokwanira zokhudza matenda osapatsirana omwe ndi kuphatizapo a shuga pofuna kuchepetsa imfa zomwe zimachitika kudzera mmatendawa
Mkulu wa bungwe la atolankhani olimbana ndi matenda a Edzi a Christopher Bauti,ndi omwe apereka pempholi m’boma la Salima, pa maphunziro a tsiku limodzi a atolankhani a momwe angamalembere nkhanizi pofuna kuzindikiritsa anthu za matendawa.
A Bauti ati pali matenda ambiri osapatsirana monga khansa, shuga ndi ena omwe akutenga miyoyo ya anthu ambiri, ndipo ati mpofunika kuti anthu azizindikiritsidwa mokwanira maka momwe angathe kuwapewera.
“Tinawona kuti ndi cha nzeru kuti tiwayitane atolankhani kuti atithandize kufalitsa uthenga wa matenda a shuga ndi ena kuti anthu azikhala akudziwa,”anatero a Bauti.
Iwo ati maphunzirowo athandiza atolankhaniwa kuti akhale ndi chinthunzinthuzi cha mmene matenda osapatsirana amayambira komanso mmene anthu odwala matendawa angasamalidwile.