Apolisi apempha anthu m’dziko muno kuti azitengera kupolisi anthu onse omwe akuwaganizira kuti apalamula milandu osati kuwalanga okha.
Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi ku Limbe mu mzinda wa Blantyre Sergent Pedzesai Zembenako ndi amene wanena izi potsatira kuphedwa kwa anthu omwe amawaganizira kuti anakaba pa malo ena ogulitsira mowa ku Chigumula mu mzindawu.
“Ndi zoona kuti anthu aphedwa chifukwa chomenyedwa ndi anthu a mmudzi. Chomwe chinachitika ndi chakuti anthuwo anapita kukaba ku Chigumula pa malo ena ogulitsira mowa atakwanisa kuba anayamba kuthawa, mwa mwayi anagwidwa ndi anthu pambuyo pake anayamba kuwamenya,” anatero Sergent Zembeneko
Sergent Zembeneko ati awiri mwa akubawo amwalilira pomwepo ndipo mmodzi anavulala kwambili ndipo wamwalilira mu njira popita ku chipatala.
Iwo ati akuyesetsa kuti athetse mchitidwewu ndipo kudzera munthambi ya chitetezo cha mmudzi tipitiliza kuwaphunzitsa mmene angachitire akagwira munthu akuba.
Pamenepa Sergent Zembeneko apempha atolankhani mdziko muno kuti agwirane ndi apolisi pophunzitsa anthu kuyipa kwa mchitidwe umenewu kamba koti umasokoneza umboni.