Pomwe apolisi mu mzinda wa Paris mdziko la France akupilizabe kuchita kafukufuku wa anthu omwe anachita chiwembu chomwe chinapha anthu pafupifupi 1 hundred 30 mdzikolo, anthu ena omwe sakudziwika ati anakawombera dera la ku mpoto kwa mzindawu.
Malipoti ati dera lomwe anthuwa anakawombera ndi limodzi mwa madera omwe zigawenga za Islamic State linawononga kwambiri pa chiwembu chomwe chinachita mdzikolo posachedwapa.
Malinga ndi malipoti a nyuzi 24 apolisi omwe amagwira ntchito pa nthawiyo avulala.
Padakali pano ndege za asilikali akhondo a mdziko la Russia ndi France zikufunafuna zigawengazi mmadera omwe akuwaganizira mdziko la Syria.