↧
Matenda a Ebola Akuyembekezeka Kutha Mdziko la GuineaMatenda a Ebola Akuyembekezeka Kutha Mdziko la
↧
Munthu wotsiriza yemwe amadwala matenda a Ebola m`dziko la Guinea wachira ndipo amutulutsa mchipatala.
Malinga ndi wofalitsa nkhani ku nthambi yomwe imayang`anira ntchito zothana ndi matendawa m`dzikolo wodwalayo yemwe ndi mwana wa masiku khumi asanu ndi atatu ndipo anabadwa kwa mayi yemwe anali ndi matenda a Ebola, atamupima zotsatira zinawonetsa kuti wachira.
Malipoti ati pakatha masabata asanu ndi limodzi opanda munthu odwala matendawa, dzikolo likhala m`gulu la mayiko omwe nthendayi yatha.
Matenda a Ebola anayambira m`dziko la Guineandipo anafalikira m`mayiko a Sierra Leone ndi Liberia ndipo anapha anthu oposa 11 sauzande kuyambira m`mwezi wa March 2014.