Dziko la Canada lati lisunga anthu othawa kwao okwana 10 sauzande ochokera mdziko la Syria chikamatha chaka chino.
Malipoti a wailesi ya BBC ati dzikoli poyamba linalonjeza kuti lisunga anthu othawa kwao okwana 25 sauzande chikamatha chaka chino.
Malinga ndi malipoti boma la dzikolo lipereka malo okhala kwa amayi, ana komanso mabanja okha.
Padakali pano boma la dzikolo lalonjeza chisamaliro chabwino pa nkhani ya umoyo komanso kuti ndege za asilikali a dzikolo ndi zomwe zikhale zikunyamula anthu kuchokera mdziko la Syria kupita mdzikolo