Bungwe la National AIDS Commission NAC lati anthu omwe anapezeka ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi sayenera kusalidwa .
Mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli a Ahmidu Tung'ande ndi omwe anena izi mu mzinda wa Zomba pomwe amakumana ndi mabungwe a boma komanso omwe si a boma pomwe amawafotokozera momwe bungweli likugwilira ntchito zake.
A Tung'ande ati ndi cholinga cha bungweli kuti pomafika mchaka cha 2020 nthenda ya Edzi idzakhale itatha mdziko muno.
Iwo alangiza azipembezo zina mdziko muno kuti asiye mchitidwe woletsa akhristu awo omwe anapezeka ndi kachilombo ka HIV kuti asiye kumwa makhwala otalikitsa moyo a ARV kamba koti munthu aliyense amene anapezeka ndi kachilomboka ali ndi ufulu womwa makhwalawa.
A Tung'ande anatinso pali ana ena omwe anabadwa ndi kachilomboka ndipo apempha makolo amene ali ndi anawa kuti aziwonetsetsa kuti nthawi zonse akuwapatsa makhwala.
Mmau ake mkulu wa zaumoyo mu mzindawu a Gomezgani Nyasulu anati pakuyenera kukhala mgwirizano wabwino pakati pa mabungwe omwe amagwira ntchito zokhudza matendawa m’bomalo.
Pomaliza a Nyasulu anayamikira bungwe la NAC kamba ka ntchito yabwino yomwe likugwira yofuna kuthetsa matendawa mdziko muno.