Bungwe lotolera magazi la Malawi Blood Transfussion Service MBTS lamemeza anthu kuti agwirane nalo manja powonetsetsa kuti zipatala za m'dziko muno zili ndi magazi okwanira komanso a ukhondo.
Mkulu wa bungweli mayi Natasha Nsamala ndi omwe apereka pempholi mu mzinda wa Blantyre pomwe bungweli limafotokozera atolankhani momwe ntchito ya chaka chino yozindikiritsa anthu pa nkhani ya kupereka magazi iyendere.
Mayi Nsamala ati nyengo ya mvula chiwerengero cha anthu osowa kulandira magazi mu zipatala chimachuluka.
Iwo ati nthawi ya zisangalalo ngozi zimachuluka kotero kuti ngati magazi akhala ochepa kapena kusoweratu, miyoyo ya anthu ochuluka imakhala pa chiwopsyezo.
Pamenepa iwo apempha aMalawi omwe ali ndi kuthekera kopereka magazi kuti apereke pa nthawiyi kuti miyoyo yochuluka ipulumutsidwe.