Bungwe la Community of Saint Egidio lati ndi lokondwa kuti tsopano lakwanitsa zaka 47 kuchokera pomwe bungweli linayamba kugwira ntchito zake zolimbikitsa moyo wa mapemphero ndi kudzipeleka pogwira ntchito zachifundo ndi zina.
Bungweli lomwe linayambira ku Rome m’chaka cha in 1968, padakali pano lili ndi mamembala oposera 60,000 ndipo lafalikira mmayiko 73 pa dziko lonse.
Pa mwambo waukulu wokondwelera ntchito za bungweli akuti kunafika ma episcope zana limodzi ochokera mmayiko osiyanasiyana a padziko lonse, omwe mwazina agawana mfundo zikuluzikulu zothandiza pa ntchito za bungweli .
Zina mwa ntchito zomwe bungweli limagwira ndi kulimbikitsa mtendere wa m’mayiko, moti mbiri imasonyeza kuti bungweli linatengapo gawo lalikulu pothandiza kuthetsa nkhondo ya pa chiweniweni yomwe inachitikapo m’dziko la Mozambique.