A ku Likulu la chipani cha Mofolo Woyera ku Rome mdziko la Italy alengeza za imfa ya Bambo Attilio Corna omwe anamwalira lachiwiri pa 10 February 2015 mu mzinda wa Bergamo mdzikolo.
Bambo Corna amwalira ali ndi zaka 91 zakubadwa atatumikira mu chipani cha Mofolo woyera kwa zaka 71.
Bambo Corna anali wansembe woyamba kukhala mphunzitsi wamkulu ku Seminale ya Saint Paul the Apostles mchaka cha 1985.
Mzimu wa Bambo Atilio Corna uwuse mu mtendere wosatha.