Sister Martha Clemence Manuel Makhasa a Chipani cha Servants of Blessed Virgin Mary (SBVM), amwalira lachisanu.
Malinga ndi akulikulu la chipanichi Sister Martha anabadwa pa 8 September 1932 ndipo malumbiro awo a mpaka kufa anachita pa 8 December 1961.
Sister Martha Clemence Manuel Makhasa kudzera m`chipanichi atumikira malo osiyanasiyana monga Nguludi, Namulenga, Limbe, Magomero, Molere, Neno, Matiya, Mulanje, Utale, Nankhunda komanso Mwanza ndipo Motto yawo ndi ‘kufuna kwanu kuchitidwe.’
Malinga ndi chipani cha SBVM, Sister Martha adzawakumbukira chifukwa cha kudzichepetsa kwawo, kudzipereka pa ntchito komanso kukhala mwa mtendere.
Mwambo woyika m`manda nthupi lawo uchitika pa 16 February 2015 ku mary view ku Nguludi motsogozedwa ndi nsembe ya ukaristia.
Mzimu wa Sister Martha Clemence Manuel Makhasa uuse mu mtendere wosatha.