Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

KUTHETSA MLILI WA HIV: KUWUNIKA UDINDO WA MPINGO PA NDONDOMEKO YA 90-90-90

$
0
0

            - Osatopa ndikuchita zinthu zabwino- (2 Thess. 3:13)

Uthenga wa HIV ndi EDZI m’chaka cha 2015

From ECM Health Commission

 

1.0 CHIYAMBI

Lero ndi lamulungu loyamba  munyengo ya Adventi. Mpingo wayamba chaka chatsopano, ulendo watsopano muchikhulupiliro.  Pamene mpingo wayamba chaka chatsopanochi, ukhala ukukumbukila tsiku la EDZI, (World AIDS day), pamaodzi ndi dziko lonse la pansi; lomwe limakhalapo pa 1 December chaka chili chonse.

Patsikuli, aboma, mabungwe a mipingo, mabungwe amadela osiyanasiyana ndi anthu mu dziko lonse la pansi amawonetsapo chidwi chawo pa mlili wa HIV komanso kutsindikapo pakufunika kodzipeleka pothana ndi mlili wa matendawa. Ngati akhristu tsikuli limatithandiza kusinkhasinkha za nthenda ya HIV ndi EDZI komanso udindo wathu pa mliliwu.

Chaka chino mutu wathu ndi “kuthetselatu: kuthetselatu kutenga kachilombo ka HIV, kuthetselatu kusankhana ndi kusalana komanso kuthetselatu imfa zodza ndi EDZI” ndicholinga chofuna kukwanilitsa ndondomeko ya 90-90-90 pothana ndi matendawa yomwe inakhazikitsidwa ndi bungwe la United Nations la UNAIDS.

Tsikuli likutipatsanso mwayi woyamikila mipingo pa ntchito yomwe ikugwira pothana ndi mliliwu komanso kuwunikilapo pa ndondomeko ya 90-90-90 yothana ndi matendawa.

 

 

 

1.1 NDONDOMEKO YA 90-90-90

Chaka cha 2014, bungwe la UNAIDS linalengeza ndondomeko yatsopano ya 90-90-90 imene yamanga maziko a nfundo ya “kuthetselatu” ndi cholinga chothetselatu ka chilombo ka HIV pofika m’chaka cha 2030.

Zolinga zawo pofika 2020 ndi izi:

  • Athu 90 mwa handiredi (100) aliwonse omwe ali ndi kachilomboka adzakhala akudziwa momwe magazi  awo ali.
  • Athu 90 mwa 100 aliwonse omwe anawapeza ndi kachilomboka azakhala akulandira mankhwala otalikitsa moyo ama ARV
  • Athu 90 mwa 100 aliwose omwe akumwa mankhwala azakhala ndi chiwerengero cha tizilombo toyambitsa matendawa chotsika kwambiri magazi mwawo.

Kukwaniritsa zolingazi pofika chaka cha 2020 kuzathandiza kuthana ndi mliliwu pofika 2030, zomwe zizathandize kubweretsa moyo ndi chuma chabwino.

2.0 KODI NDI CHANI CHOMWE CHIKUCHITIKA MDZIKO LATHU?

Malawi ndi limodzi mwa mayiko omwe akhudzidwa kwambiri ndi mlili wa HIV. Pafupi-fupi  athu 10 mwa 100 aliwonse azaka zoyambira 12 mpaka 49 zakubadwa ali ndi matendawa. Chiwerengero cha athu omwe ali ndi HIV chikutsika; kuchoka pa 55,000 muchaka cha 2011 kufika pa 34,000 chaka cha 2013. Nzokhumudwitsa kuti theka la athu omwe akutenga nthedayi ndi achinyamata azaka 15 mpaka 24 zakubadwa. Anthu ambiri omwe atenga matendawa ndi omwe ankaonedwa ngati ali pachiopsezo chochepa chotengera matendawa, mwa chitsanzo athu omwe ali pa banja komanso zibwezi zokhazikika.

 

Zinthu zomwe zikupititsa patsogolo kufala kwa chilombocha HIV dziko muno ndi izi:

  • Nchitidwe ogonana, mwachitsanzo kukhala ndi athu ogonana nawo ambiri
  • Kusiyana pakati pa amayi ndi abambo kukuyika amayi ndi atsikana pachiopsezo chochulukirapo potenga matendawa
  • Umphawi omwe ukulimbikitsa kugonana kosithana ndi ndalama.

Mukudzipereka kwake pofuna kuthesa Edzi, dziko la Malawi  lavomera kugwiritsa ntchito  ndondomeko ya 90-90-90. Nfundo zoyendetsera  matenda a HIV mudziko muno zawunikiridwaso  ndi cholinga chofuna  kukumana  ndi ndondomeko ya 90-90-90.

 

 

Pofuna kukwanilitsa ndondomekozo, Malawi akufunika kuchita izi:

                               I.            Kuunika njira zoyezera HIV komanso kuunika uphungu omwe ungaperekedwe kuti athane ndi zikhulupiliro  zolakwika zokhudzana  ndikayezedwe ka HIV, ndikulimbikitsa  anthu kuti akayezetse ndikulandira uphungu oyenera.

 

                            II.            Kuchulukitsa malo olandilirapo chithandizo ndi cholinga chochepetsa kuchulukana kwa anthu pa malo omwe amalandirirapo kale, kuphunzitsa anthu za ndondomeko yatsopano  ya 90-90-90 ndinso kuwalimbikitsa kuti ayambe kumwa mankhwala mwasanga.

 

                         III.            Kulimbikitsa anthu omwe ali ndi matendawa kuti  asamasiyire panjira kumwa mankhwalawa. Kuwalimbikitsa kudzera m’magulu, komanso kaunikidwe ka chiwerengero cha tizilombo toyambitsa matendawa m’magazi mwawo kuti aziwasinthira mankhwala mu nthawi yoyenera.

3. TIKUYENERA KUCHITAPO KANTHU.

Mpingo wa Katolika watengapo mbali pothesa matenda a HIV ndi EDZI mu njira izi:

       I.            Anali oyamba kupangitsa pulogilamu ya Home Based Care mu dziko muno pamene matendawa anangoyamba kumene.

    II.            Kukumbukira tsiku la Edzi la mulungu loyamba mu nyengo ya advent chaka chili chonse.

 III.            Inapanga njira zoyendetsera nkhani  zokhudzana ndi HIV  ndi EDZI mu mpingo. HIV/AIDS Policy

 IV.            Kulimbikitsa kupewa HIV kudzera mukudziletsa kwa achinyamata ndikukhulupilika m’banja.

    V.            Kupereka chithandizo kwa odwala mwachitsazo mankhwala otalikitsa moyo komaso kuthandiza kuchiza matenda omwe angadze kamba ka HIV kudzera muzipatala.

 

Khama la mpingo  likuonekera mu ntchito  zomwe wachita. Komabe pali zambiri zomwe mpingo ungathe kuchita pothana  ndi mliliwu makamaka potsata  ndondomeko ya 90-90-90. Nyengo  ya advent  yayamba ndi mawu anzeru ochokera mwa Khristu akuti “ndinena ndi inu khalani maso (Mariko 13:33,35). Anabwereza katatu ndi cholinga chakuti anthu amvetsetse uthenga ndikutengapo gawo.

 

 

 

 

Kuti mpingo utengepo mbali pothetsa mlili wa Edzi, ufunika  kuchita zinthu izi:

       I.            GWIRIZANO MUPINGO

Mpingo umakhala ndi magawo osiyanasiyana. Tsopano nthawi yafika  yakuti magawo onse ngati a Dayosizi, Madinale, Parishi ndi Miphakati komanso Mabungwe osiyanasiyana achikatorika agwire ntchito limodzi.

    II.            KUFIKILA MAGULU OYENELA KUDZELA MA PULOGALAMU

Kafukufuku waonetsa kuti theka la anthu omwe akutenga  matenda a HIV ndi achinyamata komanso kuti anthu am’mabanja ali pachiopsezo chotenga kachilomboka. Pakufunika  ma pulogalamu kuti afikire magulu a anthuwa. Tsopano  nthawi yakwana kuti mipingo ibweretse ma pulogalamu kuti athe kufikira anthuwa. Mwachitsazo kugwiritsa ntchito makina kuti athe kufikira achinyamata ndi uthenga wa HIV ndi EDZI.

 III.            KUGAWANA NDONDOMEKO ZA 90-90-90 MU MPINGO.

Ntchito ya mpingo wakatolika pa mlili wa HIV m’madera osiyanasiyana dzikoli ikupititsa chitsogolo njira zoyendetsera matenda a HIV ndi Edzi osangothera pakupanga njirazi. Ntchito yathu ikuyezedwa  pakukwanilitsa  zolinga  zathu  komanso pakuvomereza umunthu wa anthu amene ali ndi kachilomboka komanso omwe akhuzidwa ndi matendawa . Ntchito yathu ndiyofikira  anthu ndi chifundo komanso chithandizo kwa azimayi amasiye, ana amasiye, komanso anthu omwe ataya okondedwa awo kamba ka HIV ngati njira imodzi yokumbukira anatisiya kamba ka nthendayi.

Pamene tikufuna kukwanilitsa ndondomeko ya 90-90-90, tiyesetse kutseka mpata pakugonjetsa khalidwe  lolozana chala pa nkhani ya umphwawi, kusankhana ngakhaleso kutenga HIV. Anthu omwe anapezeka ndi kachilombo asamangokhala ndi mwayi wa makhwala okha komanso kukhala ndi moyo wangwiro ndi olomekezedwa, kuchotsa kusalana ndi kusankhana kwa athu amene ali ka chilombo.

Tikuitana magawo onse a mpingo monga ma Commission, Madinare, Maparishi, Miphakati ndi Mabugwe Achikatolika kuti aphatikize ndondomeko 90-90-90 muzochitika zawo.

V.CHIFUNDO NDI CHIKONDI

Monga mpingo, tikuyenera kuzindikira kuti “aliyese ndiwofunika kuthandizidwa”.  Ndi mawu amenewa Papa Francis akuyitana onse achikatolika ndi athu okhulupirira ndiso achifundo kuti atsegule mitima yawo kwa athu osowa kuti awathandize ngati abale awo. Akutiso kwa athu omwe akufuna kudzipeleka  pakupeleka nthawi, chuma, nzeru ndi maluso awo kwa athu ena kuti tikwanilitse zofuna za anthu ovutika.

Choncho tikuyitana ansembe ndi asisteri komanso akhristu  eni ake kuti tigwirane manja pothetsa mliliwu pofika chaka cha 2030. Tonse tigathe!

 

Wolemba

 

Mr. Carsterns Mulume                                               Mrs. Bertha Magomero

DIRECTOR OF SOCIAL DEVELOPMENT                     NATIONAL HEALTH SECRETARY


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>