Muuthenga wachaka cha achinyamata chaka chino, mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco, wapempha akhristu mumpingowu kuti azamitse moyo wawo wauzimu poyeretsa mitima yawo.
Muuthengawu Papa Francisco, wapempha akhristu makanso achinyamata, kuti akumbukire zolinga zawo za nthawi zonse pomwe amafunitsitsa kukhala moyo osangalala, ndipo walangiza kuti akonze mitima yawo kuti ayanjane ndi Mulungu yemwe angawapatse chimwemwe chomwe amafuna nthawi zonse.
Mwambo okondwelera chaka cha achinyamata, umachitika patsiku lakanjeza chaka chilichonse mumpingowu padziko lonse, ndipo mpingowu, umasonkhanitsa achinyamata mdziko limodzi kuti akondwere limodzi pakatha zaka zinayi.
Mwambo omaliza wa chaka cha achinyamata unachitikira mumzinda wa Rio de Jenairo mdziko la Brazil mchaka cha 2013 ndipo mwambo otsatira,udzachikira mumzinda wa Krakow mdziko la Poland mchaka cha 2016.