Bungwe la South Africa Medicines Control Council mdziko la South Africa lavomeleza kuti mankhwala omwe anapangidwa pofuna kupewa kutenga kwa kachilombo a HIV ayambe kugwira ntchito mdzikomo.
Mankhwalawa omwe akuwatchula dzina loti Truvada ndipo ndi ama pilisi akuyenera kumamwedwa tsiku lililonse .
Malipoti a Nyuzi 24 ati mankhwalawa athandizanso kuchepetsa chiwerengero cha achinyamata omwe ndi apakati pazaka 15 komanso 20 kamba koti ndi gulu la anthu omwe ali pachiwopsezo chotenga kachilomboka.
Malinga ndi malipoti mankhwalawa cholinga chake chinali chofuna kuti azichiza matenda a EDZI koma atayesedwa, zotsatira zapezeka kuti zithandiza munthu amene alibe matendawa kuti asatenge kachilomboka.
Mankhwala asanayambe kuperekedwa mzipatala za mdzikomo ati awona mmene angakhudzire ntchito ya zaumoyo mdzikomo.