Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Wati Maria Anawona Chifundo cha Mulungu

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati Maria mai wa mpulumutsi anaona chifundo cha mulungu kamba koti anakhala ndi pakati pa mzimu woyera.

Papa amalankhula izi loweruka ku likulu la mpingowu ku Vatican pa mwambo wa nsembe ya misa yokumbukira Maria wa ku Guadalupe.

Mu ulaliko wake Papa anati pomwe mpingo wayamba chaka cha chifundo chamulungu, anthu, mabanja komanso maiko akuyenera kukhala a chikondi komanso kulimbikitsa ntchito zachifundo pakati pao.

Papa anati palibe tchimo lomwe limalepheretsa Yesu Khristu kukhala wachifundo pakati pa aliyense.

Pa mwambowu Papa watsimikiza za ulendo wake wokayendera dziko la Mexico mmwezi wa February chaka cha mawa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>