Anthu pafupifupi makumi asanu ndi anayi afa potsatira zipolowe zomwe zinachitika mmadera atatu okhala asilikali mdziko la Burundi.
Malipoti a wayilesi ya BBC ati mwa anthu omwe aphedwawo matupi a anthu makumi atatu ndi anayi apezeka ali mu nsewu ndipo padakali pano sizikudziwika ngati chiwerengero cha matupi omwe apezeka mu nseuwo chaphatikizidwa ndi chomwe asilikali a dzikolo apeza.
Kusamvana mdziko la Burundi kunayamba pomwe Pulezidenti wa dzikolo Pierre Nkuruzinza analengeza kuti apikisana nao kachitatu pa chisankho cha pulezidenti chomwe chinachitika mdzikolo.
Malinga ndi malipoti anthu 2 hundred and 40 akhala akuphedwa kuyambira mmwezi wa May ndipo 2 hundred sauzande anathawira mmaiko oyandikana nao.