Malipoti a nthambi ya United Nations yoona za chisamaliro cha ana yapeza kuti chiwerengero cha ana 1 miliyoni a mdziko la Nigeria komanso maiko atatu oyandikana ndi dzikolo sakupita ku sukulu kaamba ka gulu la zigawenga za Boko Haram.
Malipoti a wailesi ya BBC ati sukulu zoposera 2 sauzande zinatsekedwa ndipo zina zinasandutsidwa malo okhalamo zigawengazo.
Pulezidenti wa dzikolo Muhammadu Buhari ati anauza asilikali a dzikolo kuti pomafika mapeto a mwezi uno, akhale atathana ndi zigawengazo ngakhale kufikira pano zigawengazo zikuponyabe mabomba mmadera osiyanasiyana mdzikolo.
Malinga ndi malipoti kufikira pano zigawengazi zapha anthu okwana 17 sauzande ndipo anthu oposera 2 miliyoni akusowa pokhala.
Padakali pano gulu la zigawenga za Boko Haram linafalikira mmaiko a Cameroon, Chad komanso Niger omwe ndi oyandikana ndi dziko la Nigeria.