Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco akuyembekezeka kukatsogolera mwambo wa misa ya Banja loyera ku tchalitchi lalikulu la St Peter’s Basilica lamulungu likudzali mu mzinda wa Rome.
Papa akatsogolera mwambowu pofunanso kukondwelera chifundo cha mulungu kwa mabanja pomwe mpingo wakhazikitsa chaka cha chifundo cha mulungu.
Iye wapempha mabanja pa dziko lonse kuti akachite nawo mwambowu mmatchalitchi awo komanso akadutse pa zitseko zoyera zomwe zinatsekulidwa pa tsiku lotsekulira chaka cha chifundochi.
Polankhula ndi wailesi ya Vatican Mkulu woyang’anira utumiki wa banja Ambuye Vincenzo Paglia anati chaka cha banja loyera ndi chimawunikira kufunika kwa banja komanso ndi mbali imodzi ya chiyitanidwe.