Bambo Rhodrick Zinyongo omwe amatumikira mu dayosizi ya mpingo wa katolika ya Dedza amwalira.
Malinga ndi a ku likulu la mpingowu mu dayosiziyo, Bambo Zinyongo amwalira lachitatu mmawa.
Bambo Zinyongo anadzozedwa kukhala wansembe mu chaka cha 1984.
Mwambo woyika mmanda thupi la malemu bambo Zinyongo uchitika lachisanu pa 8 January 2016 ku Bembeke Cathedral ndipo udzayamba ndi mwambo wa nsembe ya ukaristia nthawi ya 10 koloko mmawa.