Pomwe mpingo wa katolika umachita chaka cha ubatizo wa ambuye Yesu mumtsinje wa Yolodani , mtsogoleri wa mpingo wakatolika anabatiza makanda 26 ku Roma.
Papa Francisco wabatiza anawa pa mwambo wa nsembe ya ukaristia omwe unachitikira m`tchalitchi ya Sistine.
Papa wati kudzera mu ubatizo akhristu amapereka chikhulupirilo chao ku m`badwo wina.
Papa anauza makolo a anawa kuti asamayiwale kuti chikhulupirilo ndi chinthu chamtengo wapatali chomwe angasiyire ana awo.