Munthu m`modzi ati wafa ndi matenda a Ebola m`dziko la Liberia patangotha miyezi yowerengeka, bungwe la zaumoyo pa dziko lonse litalengeza kuti nthendayi yatha m`dzikolo.
Malinga ndi malipoti awayilesi ya BBC, mzimayi yemwe ndi wa zaka 30 zakubadwa wamwalira pachipatala china mu mzinda wa Monrovia momwe muli anthu ochuluka.
Dziko la Guinea lomwe ndi loyandikana ndi dzikoli mwapezeka anthu ochulukirapo omwe akudwala nthendayi.
Anthu oposa 11 sauzande ochokera m`mayiko a Guinea , Liberia, komanso Sierra Leone anafa ndi nthendayi mzaka ziwiri zapitazo.