Mpingo wa katolika mu dayosizi ya Chikwawa wapempha boma ndi mabungwe akufuna kwabwino kuti alimbikitse ntchito yosamalira anthu omwe akuvutika kamba kosowa zinthu zofunika pamoyo wao wa tsiku ndi tsiku.
Episkopi wa dayosizi ya Chikwawa Ambuye Peter Musikuwa ndi omwe anena izi pa mwambo wokhazikitsa chitukuko cha madzi a mijigo ndi zimbudzi za makono zomwe zamangidwa m`dera la Mfumu yaikulu Tengani m`boma la Nsanje.
Ambuye Musikuwa ati zitukukozi zithandiza anthu kukhala ndi madzi a ukhondo yomwe ndi njira imodzi yopewera matenda otsegula m`mimba ngati kolera omwe amakula nthawi ya mvula.