Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dziko la Kenya Lichita Mapemphero a Ophunzira a pa Sukulu ya Garissa

$
0
0

Anthu m`dziko la Kenya achita mapemphero  okumbukira mizimu ya anthu 148  omwe anafa pa chiwembu chomwe gulu la zigawenga za Al- Shabab zinachita pa sukulu ya ukachenjede ya Garisa m`dzikolo.

Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC  anthu mazanamazana anasokhana pa sukuluyo  ndipo anachita mapemphero komanso miyambo yoyatsa makandulo inachitikanso  malo osiyanasiyana kuphatikizapo mumzinda wa Nairobi ndipo inatsogoleredwa ndi akuluakulu a boma. 

Chiwembu ngati chomwechi chinachitikanso m`dzikolo m`chaka cha 1998, pomwe gulu la Al-Qaeda linaphulitsa mabomba kumaofesi a kazembe wa dziko la America m`dzikolo ndi kupha anthu okwana 213.

Magulu a zigawenga za  Al- Shabab komanso Al- Qaeda omwe kwawo ndi ku Somalia  akhala akuchita ziwembu zosiyanasiyana m`dziko la Kenya posakondwa ndi kupezeka kwa asilikali a  dziko la Kenya  mugulu la asilikali a African Union (AU) omwe akuthandiza asilikali a dziko la Somalia kulimbana ndi zigawengazo.