Ngati njira imodzi yopititsira patsogolo ntchito za Radio Maria Malawi, abwenzi a wailesiyi ku dayosizi ya Zomba ati agwira ntchito limodzi ndi otumikira a wailesiyi potolera thandizo.
Wapampando wa bungwe la abwenzi a Radio Maria mu dayosiziyi a Patrick Koloko ndi omwe anena izi ku Studio yaying`ono ya Zomba pa msonkhano wa abwenzi komanso otumikira wailesiyi omwe cholinga chake chinali kulimbikitsa ubale pakati pawo.
A Koloko ati chaka chino kuli ntchito zambiri zoti agwire zopezera thandizo monga Mariatona, Ulendo wa ndawala komanso ma Promotion zomwe ati zikufunika kuti maguluwa agwirile ntchito limodzi.
Iwo alonjezanso kuti abwenziwa azigula magetsi a Transmitter ya ku Zomba ndi cholinga choti wailesiyi isamazime m`derali.
Ndipo m`mawu ake mkulu woyang`anira Studio-yi, Mai Elizabeth Mitha ati ali ndi chikhulupirilo kuti kubwera pamodzi kwa otumikirawa komanso abwenzi awailesiyi kuthandiza kupeza thandizo lochuluka pa nthawi ya Mariatona.