Pamene mpingo umachita chaka cha lamulungu la chifundo, mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akhristu kuti akhale apostoli a chifundo kwa onse osowa.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa amalankhula izi lero pa mwambo wa nsembe ya misa pa bwalo la St Peters ku likulu la mpingowu ku Vatican.
Papa wati kukhala mpostoli wa chifundo zikutanthauza kuti akhristu akuyenera kuthandiza onse omwe akukumana ndi mavuto osiyanasiyana powathandiza kuti asendere chifupi ndi Mulungu.
Pa mwambowu Papa wapemphanso mtendere mdziko la Ukraine poganizira mavuto omwe anthu a mdzikolo akukumana nawo.
Mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu wati anthu ambiri omwe akuvutika kaamba ka ziwembu zomwe zikuchitika mmaiko a ku Europe, ndi anthu okalamba komanso ana.
Iye wati kuphatikiza kuwayikiza mmapemphero anthuwa, lamulungu la pa 24 mwezi uno chopereka chonse cha mmatchalitchi a mmaiko a ku Europe chidzakhale chothandizira anthuwa.