Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mpingo wa Orthdox Mdziko la Greece ndi Wokonzeka Kulandira Papa Francisco

$
0
0

Mpingo wa Orthodox mdziko la Greece wati ndi wokonzeka kulandira mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco paulendo wake wokayendera anthu othawa kwawo mdzikolo.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati mpingowu wati Papa anawonetsa chidwi chokayendera anthu othawa kwawo omwe akukhala pa doko la Lesbos ndi cholinga choti akamve mavuto omwe akukumana nawo.

Malinga ndi mmodzi mwa akuluakulu wa ku likulu la mpingo wakatolika Father Federico Lombard akhala akukambirana za ulendowu koma padakali pano sanakonze dongosolo.

Mpingo wa Orthodox ati unapempha Papa Francisco kuti akayendere doko la Lesbos komwe mazanamazana a anthu othawa kwao akusungidwa kamba kothawa nkhondo mmayiko a kwawo komanso kukasaka ntchito.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>