Akuluakulu a Radio Maria Malawi ayamikira abwenzi a wayilesiyi kamba kowonetsa chidwi chogwirira ntchito limodzi munyengo ino yomwe wailesiyi ikukonzekera ntchito ya chaka chino yotolera thandizo lotchedwa ‘Mariatona’
Mkulu woyendetsa ntchito za wailesiyi ku studio yaying’ono ya Limbe a Medison Semba ndi omwe alankhula izi ku Limbe pambuyo pokhazikitsa komiti yomwe yasankhidwa kuti iyendetse ntchito yotolera thandizoli.
Iwo ati potengera chidwi chomwe abweziwa awonetsa, ali ndi chikhulupiliro kuti ntchitoyi ikhala yopambana komanso yopindula.
“Zinthu zayamba bwino ndipo ndili ndi chikhulupiliro kuti anthu amene tawasankhawa, tawasankha ndi mtima onse,” anatero a Semba.
A Semba apempha anthu onse okudzidwa kuti agwilire limodzi ntchito ngati ana a banja limodzi.
Malinga ndi wapampando wa komiti yomwe yasankhidwa kuti iyendetse ntchito yotolera thandizo loyendetsera ntchito za wailesiyi ya Mariatona a Fabiano Makolija udindowu awulandira mokondwa ndipo alonjeza kuti ayesetsa kuyendetsa bwino ntchitoyi kuti wailesiyi ipeze ndalama zochuluka.
“Udindo ndawulandira ndipo ndikukhulupilira kuti ndi chithandizo cha Mulungu zonse ziyenda bwino,” anatero a Makolija.
Iwo apemphanso anthu onse omwe akuyendetsa ntchito yotolera ndalama kuti aziyendetse bwino ndi cholinga choti akhristu omwe akupereka thandizoli asakhumudwe .
Ntchito yotolera thandizoyi idzayamba pa 13 mpaka pa 15 mwezi wa May.