Mmodzi mwa akhristu mu mpingo wakatolika wapereka malo ku Radio Maria Malawi ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota ndi cholinga choti wailesiyi idzalepo transmitter yake.
Mkhristuyu Martin Mangani wapereka malowa panthawi ino yomwe wailesiyi ili mkati motolera thandizo lake lotchedwa Mariatona.
Mkuluyu wati anachiona chaphindu kuti apereke malowa ku Radio Maria kuti wailesiyi ithe kufikira anthu a m’bomali ndi maboma ena ozungulira omwe padakali pano wailesiyi siimamveka.
“Nditamvera kudandaula kwa Radio Maria makamaka panthawi inoyo akuchita Mariatona yachaka chino ndinachiona chanzeru kuti ndipereke malo oti ayikepo transmitter chifukwa ndakhala zaka 23 ndili ku Dwangwa koma Radio Maria siyikumveka,” anatero a Mangani.
Iwo apemphanso akhristu a mpingo wakatolika komanso a mipingo ina kuti athandiza wailesiyi kamba koti ikukumana ndi mavuto osiyanasiyana.
A Mangani ati, “ambiri amaona ngati kuthandiza Radio Maria ndikutenga madzi mu ndowa kuthira mu nyanja pomwe sichoncho ayi.”
“Ife amene tili mkati mwa mpingo umenewu timadziwa kuti Radio Maria imasowa zambiri komanso ma pologalamu ake amathandiza pa umoyo wa munthu, wa uzimu komanso pa umoyo omwe tidzakhale nawo tikazachoka dziko lapansi pano,” anatero Mangani.
Mmawu awo Bambo Joseph Kimu omwe ndi mkulu woyendetsa ma pologalamu pa wailesiyi athokoza a Mangani pa chifundo chomwe awonetsa ku waillesiyi .
“Ife tinali okondwa kwambiri kumva kuti pali munthu amene atamva kuti Radio Maria ikufuna malo oti izalepo transmitter ku Dwangwa iye anati apereka malowo mwa ulere.
Iwo anati sakuchita mantha ndi kuchuluka kwa ndalama zomwe zikufunika pantchitoyi ponena kuti muzaka 17 zapitazi chikhazikitsireni Radio Maria yakhala ikukula ndipo ikukwaniritsa zolinga zake podalira Mulungu kudzera mwa anthu amene amayikonda.