Mtsogoleri wa dziko la Djibouti a Ismail Omar Guelleh wapambananso pa chisankho chomwe chinachitika m`dzikolo masiku apitawa.
Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC, a Guelleh apeza mavoti 87 pa 1 hundred aliwonse pa chisankhocho chomwe zipani zotsutsa boma komanso magulu omenyera ufulu wa anthu ati sichinayende bwino.
Mkuluyu ati amayembekezeka kupikisana ndi anthu asanu koma zipani zitatu zinanyanyala.
Zipani zotsutsa ati zimadandaula kaamba koti apolisi amachita nkhaza komanso nyumba zofalitsa mawu zimalemba nkhani zachisankho mokondera .
A Guelleh anayamba kulamulira dzikolo kuyambira m`chaka cha 1999.