Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati mabanja okhazikika amakhala opindula kamba koti amachititsa kuti anthu azikhala bwino mmadera komanso ana amakula ndi chikondi, makhalidwe abwino ngakhalenso kukhala bwino ndi anzawo.
Papa Francisco walankhula izi mu kalata yokhudza banja yomwe watulutsa yotchedwa ‘Chikondi cha M’banja’.
Kalatayi yati mpingo sukuyenera kuchita tsankho ku mabanja omwe akusemphana ndi chiphunzitso cha mpingo, koma ukuyenera kuwachitira chifundo komanso kuwaunikira.
Kalatayi yomwe yamanga mfundo za misonkhano ya sinodi ya ma episkopi ya mchaka cha 2014 ndi 2015, yawunikiranso achinyamata kufunika kokonzekera bwino asanalowe m’banja.