Wapampando watsopano wa bungwe la amayi mu mpingo wakatolika mu dayosizi ya Zomba , Mayi Elizabeth Meke wati komiti yawo ipitiliza kudzipeleka pa ntchito zotukula dayosiziyo.
Mayi Mekeanena izi potsatira kusankhidwa kwawo kachiwiri pa udindowu. Iwo ati udindowu awulandira ndi manja awiri kaamba koti ndi mulungu amene waasankha kuti amutumikire.
“Azimayi andikhulupilira pondisankhanso kukhala chair lady wa bungwe la amayi mu dayosizi ino ya Zomba. Pali zambiri zomwe takonza kuti tichite potukula bungwe lathu komanso dayosizi yathu. Pakadali pano tili ndi ndalama zosachepera 1 million koma tikufuna tikhalenso ndi njira yathuyathu yotithandiza kupeza ndalama,” anatero Mayi Meki.
Iwo anapempha anthu akufuna kwabwino kuti athandize bungwe lawo kuti athe kupeza minibus yoti idzichita malonda omwe ndalama zake zizikhala za bungweli.
Mmodzi mwa amayi wa anati anasankhanso Mayi Meki kamba koti amagwira ntchito zawo mbungweli modekha, modzichepetsa komanso mwa chikondi ndipo anafuna kuti izi zipitilire.
Mayi Meki akhala pa mpandowu kwa zaka zitatu ndipo akhalanso pa mpandowu kwa zaka zitatu zina.