Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mpingo wa Anglican Ukulimbikitsa Maphunziro a Atsikana

$
0
0

Mpingo wa Anglican mu dayosizi ya Uppershire kudzera mu project yomwe mpingowu unakhadzikitsa ya Msamama Community Intergrated wati upitiliza kudzipeleka polimbikitsa maphunziro atsikana.

Mkulu woyendetsa ntchito mu projectyi a Victor Mnenemba wanena izi pa bwalo la sukulu ya primary ya Nsamama m’dera la mfumu yayikulu Mponda m’boma la Mangochi pomwe mpingowu kudzera mu mu project yi umakapeleka sukulu uniform ndi makope kwa atsikana a pa sukuluyi. Iye wati mpingowu kudzera mu projecti yi wapeleka katunduyi pofuna kulimbikitsa maphunziro a atsikana pa sukuluyo ndi m’madera ena m’bomalo.

“Tapereka makope, nsapato, zikwama za ku sukulu komanso uniform ndi cholinga choti choti tiwalimbikitse atsikanawa kuti tichepetse kusiyira sukulu panjira, kukwatiwa adakali achichepere komanso kuchepetsa umphawi pakati pawo makamaka kuti alimbikire maphunziro awo,” anatero a Mnenemba.

Polankhula moyimira makolo pa sukulu yi a Augastine Msungawana omwe ndi a Headmaster a pa sukulu yi alangiza makolo kuti azidzipeleka polimbikitsa maphunziro a atsikana ndi kuti atsikana ambiri azichita bwino pa maphunziro awo mdelaro.

Project yi ndi ya ndalama zosachepera 2.5 million ndipo ndi ya zaka zinayi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>