Episkopi wa dayosizi ya Mangochi olemekezeka Ambuye Montfort Stima ayamikira asisteri achipani cha Daughters of Mary Immaculate (DMI)kamba kolimbikitsa zitukuko zosiyanasiyana mu dayosiziyo.
Ambuye Stima alankhula izi pa mwambo wotsekulira holo ya pamwamba imene asisteriwa amanga ndi cholinga choti akhale malo okumanilana ndi magulu osiyanasiyana omwe amawalimbikitsa luso la ntchito zosiyanasiyana m’madera omwe akugwilamo ntchito zawo.
“Holo yi ndiyofunikira kwambiri chifukwa ithandiza amayi ambiri kukweza miyoyo yawo kudzera mu ntchito zomwe asisteri a DMI aziwaphunzitsira mu holoyi. Aziphunzira luso loti azikhala ozidalira mmabanja mwawo,” anatero Ambuye Sitima.
Ambuye Sitima ati Holoyi sithandiza Diocese ya Mangochi yokha koma ithandizanso pa chitukuko cha dziko lonse la Malawi kamba koti asisteri wa sakuyang’ana mbali pophunzitsa luso losiyanasiyana ndipo ati asisteri wa akugwirana manja ndi boma pogwira ntchitoyi.
Mmodzi mwa akuluakulu oyendetsa ntchito za asisteri wa Sister Vasanta anati ndi okondwa kuti tsopano chipani chawo chakwanitsa khumbo lomanga malowa zomwe zithandize kuti ntchito za asisteriwa polimbikitsa chitukuko cha amayi kudzera mbungwe lawo la DMI-Womens World ziziyenda bwino.
Pothililaponso ndemanga pa zakumangidwa kwa malowa BamboBenjaminia chipannichaansembe chaMissionary of Mary Immaculateanayamikilanso asisteri wakaamba kolimbikitsa ntchito zothandiza pa chisamaliro ndi chitukuko cha anthu ozungulira sukulu ya DMI kumene asisteri wa amakhala.