Mpingo wakatolika mdziko la Nigeria wati boma la dzikolo likuyenera kuchita zokambirana ndi zigawenga za gulu la Boko Haram ndi cholinga chofuna kupulumutsa atsikana 2 hundred a mtauni ya Chibok omwe anagwidwa ndi zigawengazi mchaka cha 2014.
Kadinala John Onaiyekan ndi yemwe walankhula izi potsatira kanema yemwe zigawengazi zatulutsa yemwe akuonetsa ena mwa atsikana omwe anagwidwawa.
Iye wati boma la dzikolo kupatula kugwiritsa ntchito asilikali pofuna kuthana ndi zigawengazi, likuyenera kupeza njira zina pofuna kupulumutsa atsikanawa ndi anthu ena omwe akusungidwa mokakamiza ndi zigawengazi.
Kadinala Onaiyekan wati ndi zinthu zochititsa manyazi ku dzikolo pamene tsopano patha zaka ziwiri atsikanawa ali mmanja mwa zigawengazi, koma akulephera kuwapulumutsa.