Anthu pafupifupi asanu ndi anayi afa ndipo ena avulala m’dziko la Japan kaamba ka chivomerezi chomwe chagwedeza mthaka ya dzikolo.
Malingana ndi malipoti a wailesi ya BBC anthu ochuluka anathawa m’nyumba zawo ndipo ena anakagona mtauni ina yoyandikana ndi komwe ngoziyi yachitika. Padakali pano ntchito yopulumutsa anthuwo ati ili mkati.
Pali chiyembekezo chakuti chiwerengero cha anthu omwe afa pa ngoziyo chikhoza kukwera kaamba koti anthu ambiri avulala kwambiri chifukwa chophinjidwa ndi zipupa za nyumba zomwe zagwazo.