Arkidayosizi ya Blantyre mu mpingo wa Katolika yayamikila mgwilizano ndi luntha lomwe bungwe la mabanja a chi khristu la Christian Family Movement (CFM) ku parishi ya St Pius likuonetsa potenga mbali pa ntchito yothandiza kukonzanso Nyungwi Parish yomwe inakhudzidwa ndi ngozi ya moto.
A Vicar General a Akidayosizi-yi, Bambo Boniface Tamani ndiwo anena izi mmalo mwa mpingowu.
Iwo ayamikira bungwe la mabanjali kamba kothandiza pa ntchitoyi ndi ndalama zokwanira 3 hundred thousand kwacha.
Wapampando wa bungwe la mabanjali ku St. Pius a Aidan Gumeni ati bungwe lawo ndilokhuzidwa ndi ngoziyi nchifukwa chake atenga nawo mbali pa ntchito yokonzanso tchalichili.