Episkopi wa dayosizi ya Dedza ambuye EmmanuelKanyamawapempha achinyamata kuti akhale ndi udindo waukulu podzipeleka pa ntchito zotumikira mpingo kudzera mmautumiki osiyanasiyana.
Ambuye Kanyama anena izi pa mwambo waukulu wa tsiku la mulungu la chiyitanidwe (Vocation Sunday).
Iwo ati achinyamata mu mpingo wakatolika akuyenera kudzipereka potumikira mpingo kamba koti ndi atsogoleri a lero ndi masiku onse.
Patsikuli mwambo wa mtunduwu mdziko muno, unachitikira ku Limbe Cathedral mu arkidayosizi ya Blantyre komwe kunafikanso akuluakulu aku likulu la mpingowu ku Roma. Polankhula pa mwambowu Episkopi wa Arkidayosiziyo Ambuye Thomas Luke Msusa apempha achinyamata kuti akonde kupemphera kuti Mulungu awaululire chiyitanidwe chawo.
Ambuye Msusa ati achinyamata akuyenera kuvomera kuchiyitanidwe chawo ndi mtima wawo onse zomwe ziwathandize kukhala muchiyitanidwe chawo mokondwa ndi modzipereka.
Iwo ati mpingo ukukula ndipo atumiki ochuluka akufunika omwe azathandiza akhristu kulandira ma sakramenti komanso uphungu wa chikhristu.
Mwambowu umachitika pa dziko lonse, chaka chilichonse lamulungu la chinayi munyengo ya Pasaka.