Parishi ya Lirangwe mu Arkidayosizi ya Blantyre ya mpingo wa katolika yati ntchito yosintha kaganizidwe ka achinyamata ati ingatheke ngati pangakhale maphunziro a pafupipafupi kwa achinyamatawa.
Bambo mlangizi wa achinyamata mparishiyi bambo Jean Marie ndi omwe alankhula izi pambuyo pa maphunziro a masiku awiri omwe parishiyi inakonzera achinyamata ndi cholinga chowakumbutsa udindo wao mumpingo ndinso chitukuko cha moyo wawo.
“Maphunziro amenewa tinawayamba mu 2013 ndi pologalamu yoti tisinthe metanoya; umphawi 0, ulesi 0, chibwana 0. Pofika 2016 tikuona kuti zinthu zikusintha ndipo tikukhulupilira kuti zipitilira kusintha tikakhala kuti tikumachitachita maphunziro amenewa,” anatero Bambo Marie.
Catherine Mkwate, mmodzi mwa achinyamata omwe anachita nawo maphunzirowa anayamikira maphunzirowo ponena kuti asintha miyoyo yawo ya uzimu.
“M’mbuyomu sitimazndikira kuti akati chinyamata ndi chani tsono pano tazindikira kuti chinyamata ndi komwe kumayambira chikhristu chathu,” anatero Mkwate.
Cholinga cha maphunziro a metanoya ndikuthetsa ulesi,uphawi ndi chibwana pakati pa achinyamata.