Achinyamata a kwa Mayaka m’boma la Zomba akuyimba lokoma ndi luso la ntchito zosiyanasiyana zomwe aphunzira kuchokera ku nthambi ya za maphunziro mu mpingo wakatolika mu dayosizi ya Zomba.
Achinyamatawa ayamikira bungweli pa bwalo la sukulu ya pulayimale ya St. Martin m’delaro pa zochitika-chitika za nthambiyi pomwe achinyamatawa anapatsidwa mwayi woti awonetse luso la ntchito zosiyanasiyana zomwe akhala akuphunzira ndi upangiri wa nthambiyi.
Malinga ndi mkulu woyendetsa ntchito mu nthambi ya maphunziro mu dayosizi ya Zomba mayi Faith Themba, nthambiyi yakhala ikuphunzitsa achinyamatawa ntchito za luso zosiyanasiyana kwa nthawi yaitali.
Iwo anati maluso osiyanasiyanawa athandiza achinyamatawa kukahala odzidalira pa moyo wawo.
Achinyamatawa ndi a zaka zoyambira 10 mpaka 35 ndipo ntchitoyi ikugwiridwa ndi thandizo la ndalama zochoka ku bungwe la Save the Children.