Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

ECM Yapempha Komiti Ya Ophunzira Msukulu Zachikatolika Zaukachenjende Kukwaniritsa Mfundo Zake

$
0
0

Komiti yatsopano ya bungwe la ophunzira achikatolika a msukulu za ukachenjede m’dziko muno   ayipempha kuti idzipeleke pa ntchito zotukula bungweli m’dziko muno.

Mlangizi wa achinyamata ku likulu la mpingo wakatolika m’dziko muno la Episcopal Conference Of Malawi(ECM)  Bambo Vincent Mwakhwawa anena izi potsatira msonkhano umene anali nawo ndi atsogoleri a bungwe la ophunzira achikatolika-wa mdziko muno.

A Mwakhwawa ati atsogoleri  atsopano a bungweli akuyenera kudzipeleka kwambiri ndi cholinga choti bungweli lipitilire kukhala la chikoka pakati pa ophunzira ambiri achikatolika msukuluzi. Iwo apempha bungweli kuti lionetsetse kuti lakwaniritsa mfundo zomwe achinyamata anakonza pamkumano wawo wa masiku atatu omwe unachitikira ku Salima zokhuza kusamalira chilengedwe, kupemphera ndi kulimbikitsa moyo wachikatolika msukulu zawo.

Polankhulapo pulezidenti watsopano wa bungweli Emmanuel Kafulafulawati komiti yawo iyetsetsa kukhala yogwilizana kuti ikwanitse ena mwa mapulani ake mzaka zomwe ikhale ikutsogolera bungweli mdziko muno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>