Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la Maneb Lapempha Magulu kuti Adzipereke

$
0
0

Bungwe lowona za mayeso mdziko muno la National Examinations Board MANEB,lapempha magulu osiyanasiyana kuti adzipereke powonetsetsa kuti vuto lobera mayeso lipitilire kuchepa mdziko muno.

Mkulu owona zachitetezo ku bungweli a Robert Harawa apereka pempholi lachitatu pa msonkhano wa akonzi ankhani ochokera mnyumba zosiyanasiyana, omwe unachitikira mu mzinda wa Lilongwe.

Iwo ati mu chaka cha 2014 panalibe mchitidwe wobera mayeso nthawi yolemba mayeso isanakwane, ndipo lapempha nyumbazi kuti zipitirize kuchitapo kanthu kuti nkhani yabwinoyi ipitilire.

Polankhula pa msonkhanowu a Harawa ati ndi zosangalatsa powona kuti chiwerengero cha milandu yobera mayeso chinayamba kutsika mchaka cha 2002, mwa zina chifukwa chokhazikitsa njira zosiyanasiyana zoyendetsera mayeso kuphatikizapo njira yoyika pamodzi ophunzira a msukulu zingapo polemba mayeso  yotchedwa Cluster System pa chingerezi.

Iwo ati mchaka cha 2014 kunalibe nkhani yokhudza kubedwa kwa mayeso nthawi yolemba mayeso isanakwane ngakhale pena ndi pena ophunzira komanso anthu ena anagwidwa akubera mayeso.

A Harawa ati padakali pano ntchito yokonzekera  mayeso a standade 8, fomu 2 ndi 4 zafika kumapeto ndipo ophunzira 290 sauzande a standade 8 ndi omwe akuyembekezeka kulemba mayesowa kuyambira pa 6 mwezi wa mawa.

Iwo atsimikizira a Malawi onse kuti bungweli lachita chotheka kuti mayeso akayamba kulembedwa athe bwino ndipo ayika njira zosiyanasiyana zachitetezo pofuna kupewa mchitidwe obera.

Pa msonkhanowu bungweli lapempha nyumba zolemba nkhani kuti zidzipereke potenga mbali pa nkhani za chitetezo cha mayeso ndi cholinga choti dziko lino lizikhala ndi atsogoleri oyenera kutsogolera anthu kupyolera mmaphunziro awo ovomerezeka.

Pa msonkhanowu mtsogoleri wa bungwe la atolankhani la MISA MALAWI a Thom Khanje anawunikira anthu zakuyipa kobera mayeso popereka chitsanzo cha mwana yemwe adayamba kubera mayeso ali standade 8 mpaka fomu 4 kuti sangalephere kuba atalembedwa ntchito m’boma.

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>