Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Zuma wati Dziko Lake ndi la Mtendere

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la South Africa Jacub Zuma wati anthu amene amachitira alendo ziwembu mdzikolo ndi ochepa kwambiri poyerekeza ndi anthu omwe amakonda mtendere.

Pulezidenti Zuma wanena izi lachisanu pamsonkhano wa nthumwi zoyimilira anthu a mmayiko ena omwe akukhala mdzikolo omwe iye anayitanitsa.

Iye anayitanitsa msonkhanowo pofuna kumva madandaulo awo,komanso zomwe boma lake likuchita pofuna kuthetsa ziwembu zomwe mzika za dzikolo zikuchitira alendo.

Iye wapempha nthumwizo kuti zigwirane manja ndi boma lake pantchito yolimbana ndi ziwawazo.

Pakadali pano mayiko osiyanasiyana kuphatikizapo dziko lino,akupitiliza kusamutsa mzika zawo mdzikolo pofuna kupewa ziwembu zomwe akuchitiridwa.

Anthu asanu ndi awiri ndi omwe atsimikizika kuti aphedwa paziwembu zomwe zinabuka sabata zitatu zapitazi mu mzinda wa Durban ndi matauni ena.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>