Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Radio Maria Malawi Ipambana pa Nyimbo ya Mariatona

$
0
0

Radio Maria Malawi yapambana mu mpikisano wopeka ndi kujambula nyimbo yofalitsa uthenga wa Mariatona wa chaka chino mmawailesi a Radio Maria amu Africa.

Nyimbo yomwe inapekedwa ndi kuyimbidwa ndi mmodzi mwa otumikira ku Radio Maria Malawi, Funghai Mutsinze, ndi yomwe yapambana kuposa wailesi zina zonse za mu Africa.

Mmodzi mwa akuluakulu aku likulu la Radio Maria pa dziko lonse ku Rome m’dziko la Italy a Framchesio Palasios alengeza uthenga wakupambana kwa Radio Maria Malawi mu mpikisanowu.

A Palasios anati nyimbo zomwe zinatumizidwa ku likulu la wailesiyi ku Rome kuchokera mmaiko osiyanasiyana a ku Africa, nyimboya ku Malawi ndi yomwe inapekedwa mwaluso kuposa zina zonse mu mpikisanowu.

Mwa zina iwo ati yemwe wapeka ndi kuyimba nyimboyi, Funghai Mutsinze,akakumana ndi mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse lapansi Papa Francisco.

Polankhulapo mkulu woyendetsa ma pologalamu kuwailesiyi Bambo Joseph Kimu anati ndi wokondwa kuti wailesi yawo yapambana pa mpikisanowu komanso kuti akuyembekezera kulandira madalitso ochokera kwa a Papa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>