Nduna ya a papa m’mayiko Malawi ndi Zambia, Arch-Bishop Julio Murat yati ndi yokhutira ndi momwe chipembedzo cha mpingowu chikuyendera mu dayosizi yaMangochi.
Ambuye Murat anena izi ku Mangochi Cathedral pomwe amalankhula kwa atsogoleri a mpingo ochokera m’maparish ndi m’madinale opezeka mu dayosiziyi.
Iwo ati kwa masiku atatu omwe akhala akucheza ndi kuyendera malo osiyanasiyana mu dayosiziyi ndi okondwa ndi momwe mpingo wakatolika ukudzipelekera pa ntchito zosiyanasiyana.
Polankhulapo woyimira akhristu eni ake mu dayosiziyi a Linga Mowa anathokoza ndunayi kamba kofika ndi kudzacheza ndi akhristu a mu dayosiziyi.
A Linga ati zomwe ndunayi yachita ndi zinthu zamtengo wapatali ndipo zapereka chilimbikitso kwa akhristu mu dayosiziyi kuti mpingo wakatolika pa dziko lonse umawakumbukira mu zambiri.
Polankhulapo episkopi wa dayosiziyi Ambuye Montfort Stima anayitana ndunayi pamwambo wa chikondwelero chankhoswe yadayosiziyo chomwe chimakhalapo mmwezi wa October.
Ambuye Murat asanafike mu dayosizi ya Mangochi anayenderanso ntchito zamadayosizi ena ampingowu mdziko muno.